Vote For This Song
Lyrics
1st Verse Amakhala muchi nyumba cho dulaPanjapo ayimika zima galimoto Wana akhupunzira ku Bishop McKenzie Makolo adawagulira farm ku Mchinji Inu mukamuona mukumusilira Simukulakwa, munthu ndi wosilirayo Komano bvuto muli nalo inuyo Mwati lero ndi lero mufanane naye (Chorus x 2) Musamangomuona chonchi uyu (chonchi uyu x2)Adayamba monyozeka, wabvutika zaka zambiri Musamangomuona kunjoya, sagona, sapuma Inu mukuliza mkonono, akukama mkaka Hardworker! 2nd Verse Achinyamata ambili masiku anoSitivomela zomwe moyo watipatsa Kuba ndalama za boma, cashigeti Mwagulitsa mitengo yathu kwama Chadi Mukupha Njobvu kugulitsa Ivory Lero mukugulitsa munthu mzanu albino Chili chonse mungofuna chachi dule Komatu olemera mukanawafunsa (Chorus x 2) 3rd Verse Bvuto lomwe tili nalo a MalawiTimafuna ndalama zitali zitali Komatu chuma sichibwera pa kamodzi M'mwenye akulemera ndi ma freezes Mwafooka, ma Barbershop timawakana Anzathu ma Burundi akudyera momwemo Tili ndi zambiritu zolemeretsa Malo molimbikira tingofuna kuba (Chorus x 2) Bridge Mwapindula chani inu abale inu anzangaInu kulemera, kusaukitsa dziko Chokoma ndi chani kulemera mwadzidzidzi Koma mapeto ake kukathera kundende (Chorus x 2) |
Songwriters
Lucius BandaSharing is cool
You may also like...
Mobile Site
Review
Comments
46568 Plays. | 52845 Downloads.
« Nthungululu | Thank You Songs |