Vote For This Song

Lyrics

Intro:
Swag Ya Chimimba.. Indeee!
Blakjak, Indeee!
V2, I see You....
Hehehehehe..... Go Soh!

Verse One:
Ibwere Mbuzi, Tidye Pano
Zibwere Nthumbwana, Tidye Pano
Abwere Mang'ina, Tidye Pano
Libwere Linunda Ndati tidye Pano
Ibwere Liver, Tidye Pano
Ibwere Nkhumba, tidye Pano
Ibwere Sheen, Tidye Pano
Ibwere Nkhuku, Tidye Pano
Mowa Ubwere, Timwe Pano
Ndati mowa Utaa? (Ubwere Timwe Pano!!)
Akuti Komatu, Ukunenepa M'bale...
Zimenezotu Paja Ndinanena Kale!

Chorus
Ngati Uli Ndi Chimimba
Gwedeza Chonchi, Njanjitsa Chonchi, Pukusa Chonchi/
If you Have a Big Belly Just..
Shake it Like So, Flash It Like So, Wiggle It So/
Akakufunsa Uzingoti awa..
Manda A Khuku'tu(Indee)/ Usayese Chibuku'tu
Akakufunsa Uzingoti awa..
Manda A Khuku'tu(indee)/ Usayese Chibuku'tu

Verse Two:
Ngati Ulibe Chimimba, Iwe Si Deal
Uphanene Njibwa Daily Ukadya Mpilu
Akuti Nyama Simakoma, Za Usilu
Hahahaha Ala! Zausilu..
Ati Ine Nkhumba Sindidya, Iwe Si Deal
Ine Nthumbwana sizikoma, Iwe Si Deal
Kodi Linunda Mumamva Kukoma Cha, Iwe Si Deal
Ine Mang'na Amandiwopsya, Iwe Si Deal
Nkhuku ya Boil Imalimba, Iwe Si Deal
Ine Kalulu amandiwenga, Iwe Si Deal
Ati nyama ili ndi Matenda, Iwe Si Deal
Ase,, Mwina Ukupenga! Wamva? Deal

Chorus:
Verse Three:
Malo Azakudya Za Nkhwiru Sitisowa
Anatiloweza Mayina Tikafika Sitibowa
Pazodetsa Pa Nkhuku Yawilitsa, Sitisowa
Pa Kanjedza Pa Utipia Pa Mang'ina, Sitisowa
47, Majestic, Pa Nkhunda, Sitisowa
Ginnery Corner, Pa Kudya, Pork shop, Sitisowa
Pa Makhetha, Pa Mbuzi Ndi Nthumbwana, Sitisowa
Pa chikondi Stopover Pa Balaka, Sitisowa
Pa Chesterfield, 18, Pa Mdyomba, Sitisowa
Pa Bwandilo Pa chimake Pa Zinyama, Sitisowa
Pa Zalewa Road Block Umadziwa, Sitisowa
Titha Kumangodya Nyama Mpaka Dzuwali Kulowa!

Chorus:
Repeat Chorus:

Outro:
Indee!
Next Level Music
V2, Blakjak, Indee!
Go so!
Am Out...

‪#‎Composed‬ by Blakjak for Che-Kalonda Album


Songwriters

Blakjak

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Comments
Hits 20139 Plays. | 12694 Downloads.
« Wandidokonya Indetu Songs Mulibe Nkhani (Feat Blasto) »

Follow Malawi Music on Instagram