Vote For This Song

Lyrics

Akangomveka pa radio mayii taputa nkhondo Ukangoyesa kuyamikira ndiye wapalamula, Kuchoka day imeneyo chilichonse ungankambe sazakumva Akuti anafikapo atchuka moti akuzimva Mudzipatsiranji umphawi moyo umafunika kulimbikira Kumalephera kulima kumati ine mzikaimba Munakakhala a dziko lina tinakati tsiku lina mwina Koma as long as muli ku Malawi aman mudzavutika Ayi please guys musakhale osalira Anatukuka ndi nyimbo am telling you ndi anthu olimbikira Amathamanga ndi sound, kwinaku ntchito nkumagwira ' fukwa amadziwa kuti kusiya vepi zinthu ziaipira Umamopa mmalawi azikunyoza eti? samagonja Atakunyoza zaka 50 iye sadzatopa Akupezera chifukwa mpaka iwe kufooka Nkakhala ine mmangoti kambani zanu mudzatopa nokha. Nanga kungachele ife Tima spita ma bars, Hah! osakamba nkhani zina bwanji? Chorus Akunamizana kuti ndiotchuka - Eeh tinawamvapo daily amativuta Kumadzipopa kumati ife ndi a nthutha - Inde amatama koma alibe khusa - Ndinawaudza kuno ndi kumalawi - Iwo amadziika mu levels ya ma rappers a ku USA Nanga bwanji pa DFB samafika? iih sinanga ndi la ma rappers ongolira ndi mtima. (Pepani) Ati ndiotchuka kuwapasa moni satiyankha Tikaapanga 'Hi' pa Instagram sapanga reply Ati ndipatali sangacheze ni munthu wamba Takumvani ndinu otchuka koma mulibe ndalama Mukakhala kumbali kodi mmadziika m'gulu ndani? Musamazizunze choncho palibe amene akukudziwani Ndinu Tecno man musamazimve u iPad Anthu Adzalephera kukuthandizani chifukwa chamakani Mumayankhula mwamatama komanso mwauchitsiru Kumati ife ndiye tinablower nanga inu? Ku blower Kwa ku Malawi man ah sidilu Umadzikakamiza kumazipopa ukudya mpiru Mpaka kulephera kulimbikira nazo ntchito kuopa aoneka kupusa Nyimbo zake ziti zomwe mukuzivutitsira? Zoti kugula CD yake lero mmawa mkukaikwilira Two three days timva kuti oyimba uja wafwifwa Chorus Akunamizana kuti ndiotchuka - Eeh tinawamvapo daily amativuta Kumadzipopa kumati ife ndi a nthutha - Inde amatama koma alibe khusa - Ndinawaudza kuno ndi kumalawi - Iwo amadziika mu levels ya ma rappers a ku USA Nanga bwanji pa DFB samafika? iih sinanga ndi la ma rappers ongolira ndi mtima. (Pepani) Amazipopa kumati iwo ndiye anafikapo Pati? Ine nkulephera kuonapo Pezani dollar kaye man kenako muzizipopa Maumboni azikhala anthu osati inu nokha Kumangothoka zopanda umboni kodi simutopa? Kapena m'makamba za ku maloto zoti sitidziona Just wait, tidzanene ndife kuti mwa blower Koma ngati simudzasintha tidzati ndiye mukubhowa Ndiye mumadziwa munthu obhowa kuti timamutrani ah? Mmmm mm mm (Kwathuku) Timamukhoma, Nkuzamumenyesa ku khopa. Kumanso kudzamuponda, Akalimbikira kukula mtima ndithu adzadziona Chorus Akunamizana kuti ndiotchuka - Eeh tinawamvapo daily amativuta Kumadzipopa kumati ife ndi a nthutha - Inde amatama koma alibe khusa - Ndinawaudza kuno ndi kumalawi - Iwo amadziika mu levels ya ma rappers a ku USA Nanga bwanji pa DFB samafika? iih sinanga ndi la ma rappers ongolira ndi mtima. (Pepani)

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Comments

From the World

Hits 885 Plays. | 213 Downloads.