Vote For This Song

Lyrics

Intro

Uthenga waife okhudzidwa
Aaaaaaaaha
Kamodzi kawili
ah king chambiecco a.k.a Zam'bongo
Yes,ka one to dem yes
Pachimkwezamau basi as always
Eeeeehe tsekulani mapilikaniro mabwana inu

Chorus

Bwana mundilembe ntchito n'dzigwirako pa gate apo
Mwinamwake mpeze kwacha pa gate apo
N'dzalimbika, n'dzachilimika bola pakutha pamwezi nane n'dzapeze cash gate
Ndufuna ntchito n'dzigwirako pa gate apo
Mwinamwake mpeze kwacha pa gate apa
N'dzalimbika, n'dzachilimika bola pamapeto pamwezi nzalandire cashgate

Verse one

Munthune n'mbuli ine nfunako kantchito
Thandizeni bwana chonde mpezenawo ka ntchito
Sin'nakapita kwina koma kuno ku capital
Akuti zagwa kuno mwina mpeze nawo kapitolo
Ndachoka kutali uko kumudzi kwa kizito
Nzagwira iliyonse kaya nzingoliiza ma pinto ooo oh yes
Akuti kuli chuma kuno, nzalimbika nzachilimika bwana I say

Back to chorus then Verse two

Chuma nchathu icho, osamachibisa aaaara
Osamatiphimba m'maso mukuzibisa aaaaara
Mukungodumpha zoona tizizi miss'a aaaaara
Tikamazikamba nkumati tapenga misa aaaara
Palowe ansembe apa achitepo misa aaaara
Mulungu awaone kumene akuzibisa aaaara
Aziwavumbulutsa nkumawapisa aaaaara charaaaa aaaaaha

Back to chorus then Verse three

Munthune n'mbuli ine chonde thandizeni
Ndipeze nawo ntchito abwana a maliseni
Kaya sindumvetsa kaya? Komano nkagwira ntchito pa gate malipiro ndi cashgate
Mbamba ine kupanda kundithandiza haaaa malizeni
Nfuna chuma ine, malinga kumudziku n'nabeledwa ndalama ndufunika kubweza

Back to chorus x2 then outro

Aaaaaaaaha, az alwez pachimkwezamau basi
Kamodzi kawili ah king chambiecco a.k.a zam'bongo
Awa anali madando a m'modzi mwa ovutika komanso mbuli yam'mudzimu
Tikhulupilira mumuthandiza uthenga wamveka
Ndithu zikomo abwana,,zimatha zimatha eeee

Songwriters

King Chambiecco, Snake J

Sharing is cool

You may also like...



Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Chambiecco, as poor people activist, chants down Cashgate in Gate man.

In Gate man, he sings about a man who has left his home village and goes to Lilongwe looking for a job at Capital Hill to work as a Security Guard (Gateman) after hearing that there is a lot of ‘cash’ at the Capital Hill.

Comments
Hits 9221 Plays. | 8133 Downloads.
« Black Out Again Singles Songs Sir Yes Sir »

Follow Malawi Music on Instagram