Vote For This Song

Lyrics

Siwamatama, siwonyada, alibe mwano

Koma akuopa poti adamputsitsa wena

Chinamuluma chakuda

Amuchulukira ndi mantha

Lero chakuda chirichonse akumangothawa

 

Chorus

Sikuti alibe chikondi

Ayi amakonda

Sikutinso safuna kukondedwa

Ayi ndithu amafuna

Koma chinamuluma chakuda

Olo aone khala amathawa

Anamukhumudwitsa ena

Sakhulupiliranso wina aliyense

Sanganame sizimampweteka

Ayi zimawawa

Akaona ena akukondana

Ndithudi amasilira

Koma chinamuluma chakuda

Olo aone khala amathawa

Anamukhumudwitsa ena

Ali ndi mantha

 

Verse 1

Achemwaliwa kodi n’chani

Ine amandidabwitsa

Nkhani zachikondi sakhudzidwa

Ngakhale mphekesera samveka

Ndikawafunsa vuto n’chani chemwa

Amangopukusa mutu

Mditafufuza ndapeza kuti

Anakhumudwitsidwapo

Anali naye wokondedwa

Yemwe iwowa amkamufera

Ankamuchitira chirichonse

Kuti mtima wake uzisangalala

Ankalola kudana ndi aliyense

Kumamukonda yekhayo

Abale ndi makolo osawamvera

Ankangomvera yekhayo

Koma anazizwa tsiku lina

Agule nyuzi aoneko nkhani

Anaona nkhope ya okondedwa wakeyo

Akulengeza za ukwati ndi wina

Mtima wake unasweka

Ndipo sanakhulupilire

Ndi chain chomwe unkasowa mwaine

Kundipanga chipongwe chotere?

Akakumbuka nyengo zonse

Wadutsa limodzi ndi okondedwayo

Akakumbukanso malonjezano

A ukwati woyera

Wasankhira kuzunza mtima’nga

Kundisandutsa chitonzo

Unandilakwira eeeh

Sindifunanso kumva za chikondi

 

Chorus

 

Verse 2

Mtima wa mzako n’tsidya lina

Akulu akale ndithu sananame

Pamaso paoneka ngati akukonda

Mumtima muli wina emwe amamukonda

Zikuchitika m’dziko muno

Sinkhambakamwa chabe

Nkhani yachikondi ikati izunze pena

Kulakalaka kuzipha

Mkulu wina adazikhweza

Nkhani zake zachikondi zomwezi

Mkazi wake ankamukonda

Ankayesetsa kumamuchengetera

Koma tsiku lina anakhumudwa

Anamupeza ndi wina

Koma olo zingatero tisaziphe chonde

Awa simathero a zonse

Ena kuchoka pomwe adakhumudwitsidwa

Moyo wawo unasokonekera

Akuti sangathenso kukonda mmodzi

Akuopa azawakhumudwitsanso

Lero chikondi amangogula

Akasiyana chathera pompo

Tsoka liri pamoyo wawo

Anauika pachiswe

Uthenga wanga kwa ena nonse

Amene sim’napeze okondedwa

Musachite mantha kupeza mmodzi

Poti chikondi adalenga ndi Jehova

Chongofunika ndi kudekha

Kudikira nthawi yanu

Azakupatseni wanu Ambuye

Yemwe adakukonzerani

Nthawi zina mavuto amabwera

Kamba ka mmene mudaziyambira

Mudamupeza kuti mudakumana bwanji

Ndipo mwa iye munkatsatanji

Ulendo wa banja ngwautali

Inu osakakamiza

Muntaye ngati alibe chikondi

Mungadzalire moyo onse

 

Siwamatama, siwonyada, alibe mwano

Koma akuopa poti adamputsitsa wena

Chinamuluma chakuda

Amuchulukira ndi mantha

Lero chakuda chirichonse akumangothawa

 

 

Usalire mlongo wanga

(usalire)

Usalire m’bale wanga

Usataye mtima

Usaononge moyo

Mpakana kudzipha

Udzampeza wina

Usacheuke

Zakale zapita uziyiwale

Pempha kwa Jehova

Azakupatsa wina

Wokonda, wosunga, wosamala

 

Chorus


Songwriters

Skeffa Chimoto

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Chinamuluma Chokuda by Skeffa Chimoto.

Comments
Hits 61665 Plays. | 13632 Downloads.
« Dalitsani Okondedwa Chikondi Songs Ndilandireni »

Join us on Instagram

LIKE MALAWI-MUSIC ON FACEBOOK

FOLLOW MALAWI-MUSIC ON TWITTER