Vote For This Song

Lyrics

Aaaaah

My babe girl

She’s so loving

She’s so patient

She’s my heavenly sent

 

CHORUS

Mbuye dalitsani okondedwa wanga

Mumpatse moyo wautali ndi wathanzi

Poti ndiye apangitsa

Moyo wanga kukoma

Ndichotsereni mtima wachimasomaso

Asamazunzike ndi kundidandaula

Poti ndiye apangitsa

Moyo wanga kuwala

Ndiye apangitsa

Moyo wanga kukoma

Ndiye apangitsa

Moyo wanga kuwala

 

VERSE 1

Kalekale okongola ndinkangowaonera patali

Kumangodzidelera kuti ine sangandilore

Malingana ndi nyengo zimene ndinali kudutsamo

Sindinkadziwa Chauta adandisungira wanga mmodzi

Lero lino siuyu ali nane pambalipa

Amakhala nane m’nyengo zanga zonse

Amalira pomwe ine ndikulira

Amasangalara pomwe ine ndiri pachimwemwe

Onena nenani koma izi zokha sim’sokoneza

Popeza ndi banja lochoka kwa Chauta

Mukatiyang’anitsitsa timayenerana timakhalana

Sizochoka kwa munthu adapereka yekha Chauta

Namalenga, Namalenga, ndikadakonda inu mukadakhala m’busa wathu

Mudzzitiyang’anira tikhale banja lachitsanzo

Akamaona ife anthu azisilira

 

CHORUS

 

VERSE 2

Ndi zomvetsa chisoni mabanja ena lero

Angokhalira limodzi koma banja linatha

Bambo amapanga zawo, amayinso zawo

Kumatukwanizana pamaso pa ana

Nthawi zina kumenyana zopanda ulemu

Palibe amafuna kulolera mzake

Koma zikakumana njobvu umavutika ndi udzu

Pamapeto pa zonse ozunzika ndi anawa

Ena amayambana akapeza chuma

Nthawi yomwe adali amphawi ankakondana

China chirichonse ankachita limodzi

Ngakhale kutchalitchi ankapita limodzi

Lero Mulungu wadalitsa walakwanso wapalamula

Lero chikondi chabambo, amayi sachiona

Ananso chikondi chamakolo ndithudi sachiona

Ayambanso kupemphera kuti bola asaukenso

Azikhalanso mwachikondi bwinobwino ngati kale

 

Aaaah

My babe girl

She’s so loving

She’s so patient

She’s my heavenly sent

 

 

CHORUS


Songwriters

Skeffa Chimoto

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Comments
Hits 53372 Plays. | 11486 Downloads.
Chikondi Songs Chinamuluma Chokuda »

Join us on Instagram

LIKE MALAWI-MUSIC ON FACEBOOK

FOLLOW MALAWI-MUSIC ON TWITTER