Vote For This Song

Lyrics

INTRO Nkadzangoti ndafika ine chongoti ndalowa koma pomdikilira oyendetsa pologalamuyo ine chongoti ndafika ine ndekha kungoti ndalowa koma pomdikilira oyendetsa pologalamuyo ine kungoti am in side koma kungoti ndalowa pomdikilira oyendetsa pologalamuyo CHORUS koma nde kudzakhala ma ma ma ine ma ma ee macheza x 2 moyo wakumwamba aa aa moyo wakumwamba aa aa moyo wakumwamba aa aa aa yes VERSE ONE kumuona yobu ali kumwamba atanenepa atasalala zosiyana ndi timanva zija ee ee koma moyo wakumwamba kumuona yohane ali kumwamba yemwe uja adam'dula mutu koma kumwamba ali nchimutu anzanga chosililitsa inu chosililitsa inu ndipite apo ndipite apo apa kagulu apo kagulu kucheza ndi mose ndi eliya oh ooo koma moyo wakumwamba moyo wakumwamba tifike apo tifike apo apa kagulu apo kagulu kucheza ndi mose ndi angelo oh oo koma moyo wakumwamba moyo wakumwamba CHORUS VERSE TWO Ndzangomva wina alukodola ine uyang'ana sinkudziwa akundifunsa what is your name ineumuza Namadingo akundiuza watanganidwa mphwanga kuno nkumwamba ukhale pansi kumafunika discipline discipline oh oo koma moyo wakumwamba moyo wakumwamba ine kukhazikika khuma ndumuona alubwelanso kachiwiri kudzandikodola eeh ee ee e koma moyo wakumwamba akundiuza pachitika misiteki malowedwe ako akuno ukayenkhe mafunso ukayankhe mafunso, ukayankhe mafunso ine ukafika pa lisepishoni ndukumana ndi mngelo wachitetezo akundifunsa bwanji nkhopeyi ukuoneka wachisoni ine umuyankha ndamva kale pachitika misiteki malowedwe anga akuno ooh oo koma moyo wakumwamba moyo wakumwamba koma iyeyu nkundimwetulira akuti usadandaule timangofuna tikutenthetse ukalowa walowa ukalowa walowa -BACK TO CHORUS- VERSE THREE Ulendo wanga kubwelela kugulu ati nkavine ati nkanjoye ati nkanyade zanga zili bwino ee ee koma moyo wakumwamba moyo wakumwamba koma panjila ine gululu ndukumana ndiwangongole adamwalira nsadampatse zake ee ee koma moyo wakumba moyo wakumwamba akundifunsa ukutani kuno iwe tambwali iwe kathyali walowa bwanji moyo wakumwamba uli ngongole yanga iwe ine umuyankha momwetulira n'damva uthenga pamaliro ako n'dapeleka moyo wanga kwa yesu adalipila ngongole zanga LAST CHORUS

Songwriters

Patience Namadingo, Amos Mlolowah

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Comments
Hits 34983 Plays. | 55637 Downloads.

Join us on Instagram

LIKE MALAWI-MUSIC ON FACEBOOK

FOLLOW MALAWI-MUSIC ON TWITTER