Vote For This Song

Lyrics

VERSE

Chomwe munthu wamkulu akuchiona atakhala pansi

Mwana sangachione olo ataimilira

Economic recovery plan Malawi yativuta

Taonani yayamba kutulutsa minga

Mfumu inatiuza kuti potha miyezi 18

Chuma cha dziko la Malawi chiyamba kuyendanso bwino

Lero tiku’uzidwa kuti Kwacha yalimba tsopano

Iri ndi mphamvu, mukunamiza mafuko

Ngati Kwacha iri ndi mphamvu bwanji mitengo ya katundu

Ikukwerabe, sikutsika mitengo

Mafuta agalimoto akumatsika mtengo

Kutsitsa akunenako atsitsa ndi K10

 

CHORUS

KULIRA KWA AMPHAWI

KWAMVEKA DZIKO LONSE

KULIBE AKUTIMVA

AYANG’ANA KUMBALI

ONSE PAGULU LAWO

AONJEZA MAKANI

ATI TIZITAKATA IFE

TITAKATA BWANJI?

POMWE TIRIBE MPAMBA

ZOMWE TIKADALIRA KALE

ZIDALEKA KUYENDA

 

VERSE

Mayiko anzathu tidayandikana nawo

Ndi otukuka, anthu ambiri alemera

Mavoti awo adasankha amuna ochita malonda, otha bizinesi

Chitsanzo ku Mozambique anthu adavotera ndani?

Armando Guebuza munthu wa bizinesi

Pa Zambia pomwepa wanthu adavotera ndani?

Micheal Sata munthu wa bizinesi

Pitani ku mayiko awo mukapeze n’kotukuka

Sungayerekeze n’pano pa Nyasaland

Nafenso a Malawi tichite chimodzimodzi

Tisankhe munthu ochita bizinesi

 

CHORUS

KULIRA KWA AMPHAWI

KWAMVEKA DZIKO LONSE

KULIBE AKUTIMVA

AYANG’ANA KUMBALI

ONSE PAGULU LAWO

AONJEZA MAKANI

ATI TIZITAKATA IFE

TITAKATA BWANJI?

POMWE TIRIBE MPAMBA

ZOMWE TIKADALIRA KALE

ZIDALEKA KUYENDA


Songwriters

Joseph Nkasa

Sharing is cool

You may also like...Mobile Site

To view this page on the Malawi-Music.com mobile site Click here

Review

Kulira kwa Amphawi is Nkasa's 1st single for his latest upcoming album which promises more fireworks and thrills. Enjoy!

Comments
Hits 48165 Plays. | 33572 Downloads.
Kulira Kwa Amphawi Songs Opani Yehova »

Join us on Instagram

LIKE MALAWI-MUSIC ON FACEBOOK

FOLLOW MALAWI-MUSIC ON TWITTER